Mateyu 2:10 - Buku Lopatulika Ndipo iwo poona nyenyeziyo, anakondwera ndi kukondwera kwakukulu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iwo poona nyenyeziyo, anakondwera ndi kukondwera kwakukulu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ataiwona nyenyeziyo, adasangalala kwabasi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene iwo anaona nyenyeziyo, anasangalala kwambiri. |
Anthu akondwere, nafuule mokondwera; pakuti mudzaweruza anthu molunjika, ndipo mudzalangiza anthu padziko lapansi.
Ndipo pofika kunyumba anaona kamwanako ndi Maria amake, ndipo anagwa pansi namgwadira Iye; namasula chuma chao, nampatsa Iye mitulo, ndiyo golide ndi lubani ndi mure.
Ndipo iwo, m'mene anamva mfumu, anamuka; ndipo onani, nyenyezi ija anaiona kum'mawa, inawatsogolera iwo, kufikira inadza nkuima pamwamba pomwe panali kamwanako.
Ndipo mngelo anati kwa iwo, Musaope; pakuti onani, ndikuuzani inu uthenga wabwino wa chikondwero chachikulu, chimene chidzakhala kwa anthu onse;
Ndipo abusawo anabwera, nalemekeza ndi kutamanda Mulungu pa zinthu zonse anazimva, naziona, monga kunalankhulidwa kwa iwo.
Anamuyendetsa pa misanje ya dziko lapansi, ndipo anadya zipatso za m'minda; namyamwitsa uchi wa m'thanthwe, ndi mafuta m'mwala wansangalabwe;