Mateyu 17:8 - Buku Lopatulika Ndipo iwo, pokweza maso ao sanaone munthu, koma Yesu yekha. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iwo, pokweza maso ao sanaone munthu, koma Yesu yekha. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iwo aja poŵeramuka, adangoona kuti palibe munthu winanso, koma Yesu yekha. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atayangʼana, sanaone wina aliyense kupatula Yesu yekha. |
Ndipo pamene anali kutsika paphiri, Yesu anawalamula iwo kuti, Musakauze munthu choonekacho, kufikira Mwana wa Munthu adadzauka kwa akufa.
Ndipo dzidzidzi pounguzaunguza, sanapenye munthu wina yense, koma Yesu yekha, ndi iwo eni.
Ndipo pakutero mauwo, Yesu anapezedwa ali yekha. Ndipo iwo anakhala chete, ndipo sanauze munthu aliyense masiku aja kanthu konse ka izo anaziona.