Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 17:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo pamene anali kutsika paphiri, Yesu anawalamula iwo kuti, Musakauze munthu choonekacho, kufikira Mwana wa Munthu adadzauka kwa akufa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo pamene anali kutsika paphiri, Yesu anawalamula iwo kuti, Musakauze munthu choonekacho, kufikira Mwana wa Munthu adadzauka kwa akufa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Pamene ankatsika phiri lija, Yesu adaŵalamula kuti, “Zimene mwaona m'masomphenyazi musakauze wina aliyense mpaka Mwana wa Munthu atauka kwa akufa.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Akutsika ku phiriko, Yesu anawalamula kuti, “Musawuze wina aliyense zimene mwaona, mpaka Mwana wa Munthu ataukitsidwa kwa akufa.”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 17:9
16 Mawu Ofanana  

nawalimbitsira mau kuti asamuwulule Iye;


koma ndinena kwa inu, kuti Eliya anadza kale, ndipo iwo sanamdziwe iye, koma anamchitira zonse zimene anazifuna iwo. Ndipo chonchonso Mwana wa Munthu adzazunzidwa ndi iwo.


Ndipo Iye ananena kwa iwo, Chifukwa chikhulupiriro chanu nchaching'ono: pakuti indetu ndinena kwa inu, Mukakhala nacho chikhulupiriro monga kambeu kampiru, mudzati ndi phiri ili, Senderapo umuke kuja; ndipo lidzasendera; ndipo palibe kanthu kadzakukanikani.


Ndipo m'mene anali kutsotsa mu Galileya, Yesu ananena nao, Mwana wa Munthu adzaperekedwa m'manja a anthu;


ndipo adzamupha Iye, ndipo Iye adzauka tsiku lachitatu. Ndipo iwo anali ndi chisoni chachikulu.


Ndipo iwo, pokweza maso ao sanaone munthu, koma Yesu yekha.


Ndipo Yesu ananena kwa iye, Ankhandwe ali nazo nkhwimba zao, ndi mbalame za m'mlengalenga zisa zao, koma Mwana wa Munthu alibe potsamira mutu wake.


Ndipo Yesu ananena naye, Ona, iwe, usauze munthu; koma muka, udzionetse wekha kwa wansembe, nupereke mtulo umene anaulamulira Mose, ukhale mboni kwa iwo.


Ndipo anawauzitsa iwo kuti asanene kwa munthu mmodzi za Iye.


Ndipo atate wake ndi amake anadabwa; ndipo analamulira iwo asauze munthu aliyense chimene chinachitika.


Ndipo pakutero mauwo, Yesu anapezedwa ali yekha. Ndipo iwo anakhala chete, ndipo sanauze munthu aliyense masiku aja kanthu konse ka izo anaziona.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa