Mateyu 13:7 - Buku Lopatulika Koma zina zinagwa paminga, ndipo mingayo inayanga, nkuzitsamwitsa izo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma zina zinagwa paminga, ndipo mingayo inayanga, nizitsamwitsa izo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mbeu zina zidagwera pa zitsamba zaminga. Zitsambazo pokula zidalanda chakudya cha mbeu zija. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mbewu zina zinagwa pa minga ndipo mingayo inayanga ndi kuzirepheretsa kukula. |
Ndipo iye amene afesedwa kuminga, uyu ndiye wakumva mau; ndipo kulabadira kwa dziko lapansi, ndi chinyengo cha chuma chitsamwitsa mau, ndipo akhala wopanda chipatso.
Koma zina zinagwa pa nthaka yabwino, ndipo zinabala zipatso, zina za makumi khumi, zina za makumi asanu ndi limodzi, zina za makumi atatu.
Ndipo zina zinagwa paminga, ndipo minga inakula, nkuzitsamwitsa, ndipo sizinabale zipatso.