Koma munatuluka kukaona chiyani? Munthu wovala zofewa kodi? Onani, akuvala zofewa ali m'nyumba zamafumu.
Mateyu 11:9 - Buku Lopatulika Koma munatulukiranji? Kukaona mneneri kodi? Indetu, ndinena kwa inu, wakuposa mneneri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma munatulukiranji? Kukaona mneneri kodi? Indetu, ndinena kwa inu, wakuposa mneneri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tanenanitu, mudaati mukaona chiyani? Mneneri kodi? Zoonadi, ndipo ndikunenetsa kuti mudakaona woposa mneneri amene. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nanga munkapita kukaona chiyani? Mneneri kodi? Inde ndikuwuzani kuti munkakaona woposa mneneri. |
Koma munatuluka kukaona chiyani? Munthu wovala zofewa kodi? Onani, akuvala zofewa ali m'nyumba zamafumu.
Eya, ndipo iwetu kamwanawe, udzanenedwa mneneri wa Wamkulukulu; pakuti udzatsogolera Ambuye, kukonza njira zake.
Ndiponso, tikanena, Uchokera kwa anthu; anthu onse adzatiponya miyala: pakuti akopeka mtima, kuti Yohane ali mneneri.