Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 11:10 - Buku Lopatulika

10 Uyu ndiye amene kunalembedwa za iye, kuti, Onani Ine nditumiza mthenga wanga pa nkhope yanu, amene adzakonza njira yanu m'tsogolo mwanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Uyu ndiye amene kunalembedwa za iye, kuti, Onani Ine nditumiza mthenga wanga pa nkhope yanu, amene adzakonza njira yanu m'tsogolo mwanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Ameneyu ndiye uja Malembo akunena zakeyu kuti, “ ‘Nayitu nthumwi yanga, ndikuituma m'tsogolo mwako, kuti ikakonzeretu njira yodzadzeramo iwe.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Uyu ndi amene malemba akunena za iye kuti, “Ine ndidzatuma mthenga wanga patsogolo panu amene adzakonza njira yanu.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 11:10
10 Mawu Ofanana  

Mau a wofuula m'chipululu, Konzani njira ya Yehova, lungamitsani m'dziko loti see khwalala la Mulungu wathu.


Taonani, ndituma mthenga wanga, kuti akonzeretu njira pamaso panga; ndipo Ambuye amene mumfuna adzadza ku Kachisi wake modzidzimutsa; ndiye mthenga wa chipangano amene mukondwera naye; taonani akudza, ati Yehova wa makamu.


Taonani, ndidzakutumizirani Eliya mneneri lisanadze tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova.


Indetu ndinena kwa inu, Sanauke wakubadwa mwa mkazi munthu wamkulu woposa Yohane Mbatizi; koma iye amene ali wochepa mu Ufumu wa Kumwamba amkulira iye.


nati kwa Iye, Inu ndinu wakudza kodi, kapena tiyembekezere wina?


Pakuti uyu ndiye ananenayo Yesaya mneneri, kuti, Mau a wofuula m'chipululu, konzani khwalala la Ambuye, lungamitsani njira zake.


Monga mwalembedwa mu Yesaya mneneri, Ona, ndituma mthenga wanga patsogolo pa nkhope yanu, amene adzakonza njira yanu.


Eya, ndipo iwetu kamwanawe, udzanenedwa mneneri wa Wamkulukulu; pakuti udzatsogolera Ambuye, kukonza njira zake.


Anati, Ndine mau a wofuula m'chipululu, Lungamitsani njira ya Mbuye, monga anati Yesaya mneneriyo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa