Ndinasochera ngati nkhosa yotayika; funani mtumiki wanu; pakuti sindiiwala malamulo anu.
Mateyu 10:6 - Buku Lopatulika koma makamaka mupite kunkhosa zosokera za banja la Israele. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 koma makamaka mupite kunkhosa zosokera za banja la Israele. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma makamaka mupite kwa Aisraele amene ali ngati nkhosa zotayika. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma pitani kwa nkhosa zotayika za banja la Israeli. |
Ndinasochera ngati nkhosa yotayika; funani mtumiki wanu; pakuti sindiiwala malamulo anu.
Tonse tasochera ngati nkhosa; tonse tayenda yense m'njira ya mwini yekha; ndipo Yehova anaika pa Iye mphulupulu ya ife tonse.
Israele ndiye nkhosa yolowerera, mikango yampirikitsa, poyamba inamudya mfumu ya Asiriya; ndipo pomaliza Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni wathyola mafupa ake.
Anthu anga anakhala nkhosa zotayika; abusa ao anazisokeretsa pa mapiri onyenga; achoka kuphiri kunka kuchitunda; aiwala malo ao akupuma.
Ndidzafuna yotayika, ndi kubweza yopirikitsidwa, ndi kulukira chika yothyoka mwendo, ndikulimbitsa yodwalayo; koma yonenepa ndi yolimba ndidzaziononga, ndidzazidyetsa ndi chiweruzo.
Zofooka simunazilimbitse; yodwala simunaichiritse, yothyoka simunailukire chika, yopirikitsidwa simunaibweze, yotayika simunaifune; koma munazilamulira mwamphamvu ndi moopsa.
Nkhosa zanga zinasokera kumapiri ali onse, ndi pa chitunda chilichonse chachitali; inde nkhosa zanga zinabalalika padziko lonse lapansi, ndipo panalibe wakuzipwaira kapena kuzifunafuna.
Pali Ine, ati Ambuye Yehova, zedi, popeza nkhosa zanga zinakhala nyama, ndi nkhosa zanga zinakhala chakudya cha zilombo zonse zakuthengo, chifukwa kunalibe mbusa, ndi abusa anga sanafunefune nkhosa zanga, koma abusawo anadzidyetsa okha, osadyetsa nkhosa zanga;
Yang'anirani kuti musanyoze mmodzi wa ang'ono awa; pakuti ndinena kwa inu, kuti angelo ao apenya chipenyere nkhope ya Atate wanga wa Kumwamba.
ndi kuti kulalikidwe m'dzina lake kulapa ndi kukhululukidwa kwa machimo kwa mitundu yonse, kuyambira ku Yerusalemu.
Ndipo Paulo ndi Barnabasi analimbika mtima ponena, nati, Kunafunika kuti mau a Mulungu ayambe alankhulidwe kwa inu. Popeza muwakankha, nimudziyesera nokha osayenera moyo wosatha, taonani, titembenukira kwa amitundu.
Koma pamene iwo, anamkana, nachita mwano, anakutumula malaya ake, nati kwa iwo, Mwazi wanu ukhale pa mitu yanu; ine ndilibe kanthu; kuyambira tsopano ndinka kwa amitundu.
komatu kuyambira kwa iwo a mu Damasiko, ndi a mu Yerusalemu, ndi m'dziko lonse la Yudeya, ndi kwa amitundunso ndinalalikira kuti alape, natembenukire kwa Mulungu, ndi kuchita ntchito zoyenera kutembenuka mtima.
Kuyambira ndi inu, Mulungu, ataukitsa Mwana wake, anamtuma kukudalitsani inu, ndi kukubwezani yense ku zoipa zake.
Pakuti munalikusochera ngati nkhosa; koma tsopano mwabwera kwa Mbusa ndi Woyang'anira wa moyo wanu.