Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 10:5 - Buku Lopatulika

5 Awa amene, khumi ndi awiriwa, Yesu anawatumiza, nawalangiza ndi kuti, Musapite kunjira ya kwa anthu akunja, ndi m'mudzi wa Asamariya musamalowamo:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Awa amene, khumi ndi awiriwa, Yesu anawatumiza, nawalangiza ndi kuti, Musapite kunjira ya kwa anthu akunja, ndi m'mudzi wa Asamariya musamalowamo:

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Anthu khumi ndi aŵiri ameneŵa Yesu adaŵatuma ndi malamulo akuti, “Musapite kwa anthu a mitundu ina kapena kukaloŵa m'mudzi uliwonse wa Asamariya ai.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Yesu anatuma khumi ndi awiriwo ndi kuwalamula kuti, “Musapite kwa anthu a mitundu ina kapena kulowa mʼmudzi uliwonse wa Asamariya.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 10:5
27 Mawu Ofanana  

natumiza akapolo ake kukaitana oitanidwa kuukwati umene; ndipo iwo sanafune kudza.


Dziko la Zebuloni ndi dziko la Nafutali, njira ya kunyanja, kutsidya lija la Yordani, Galileya wa anthu akunja,


Ndipo anadziitanira khumi ndi awiriwo, nayamba kuwatumiza iwo awiriawiri; nawapatsa mphamvu pa mizimu yonyansa;


Zitapita izi Ambuye anaika ena makumi asanu ndi awiri, nawatuma iwo awiriawiri pamaso pake kumudzi uliwonse, ndi malo ali onse kumene ati afikeko mwini.


Koma Msamariya wina ali pa ulendo wake anadza pali iye; ndipo pakumuona, anagwidwa chifundo,


ndipo anagwa nkhope yake pansi kumapazi ake, namyamika Iye; ndipo anali Msamariya ameneyo.


Ndipo Iye anaitana pamodzi khumi ndi awiriwo nawapatsa mphamvu ndi ulamuliro pa ziwanda zonse, ndi zakuchiritsa nthenda.


Ndipo anawatuma kukalalikira Ufumu wa Mulungu, ndi kuchiritsa anthu odwala.


Monga momwe munandituma Ine kudziko lapansi, Inenso ndinatuma iwo kudziko lapansi.


Chifukwa chake Yesu anatinso kwa iwo, Mtendere ukhale ndi inu; monga Atate wandituma Ine, Inenso ndituma inu.


Makolo athu analambira m'phiri ili; ndipo inu munena, kuti mu Yerusalemu muli malo oyenera kulambiramo anthu.


Chifukwa chake anadza kumzinda wa Samariya, dzina lake Sikari, pafupi pa kadziko kamene Yakobo adapatsa mwana wake Yosefe;


Pamenepo mkazi wa mu Samariya ananena ndi Iye, Bwanji Inu, muli Myuda, mupempha kwa ine kumwa, ndine mkazi Msamariya? (Pakuti Ayuda sayenderana nao Asamariya).


Chifukwa chake Ayuda anati mwa iwo okha, Adzanka kuti uyu kuti ife sitikampeza Iye? Kodi adzamuka kwa Agriki obalalikawo, ndi kuphunzitsa Agriki?


Ayuda anayankha nati kwa Iye, Kodi sitinenetsa kuti Inu ndinu Msamariya, ndipo muli ndi chiwanda?


Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ndi mu Yudeya monse, ndi mu Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.


Ndipo anadabwa okhulupirirawo akumdulidwe onse amene anadza ndi Petro, chifukwa pa amitundunso panathiridwa mphatso ya Mzimu Woyera.


Ndipo Saulo analikuvomerezana nao pa imfa yake. Ndipo tsikulo kunayamba kuzunza kwakukulu pa Mpingo unali mu Yerusalemu; ndipo anabalalitsidwa onse m'maiko a Yudeya ndi Samariya, koma osati atumwi ai.


natiletsa ife kuti tisalankhule ndi akunja kuti apulumutsidwe; kudzaza machimo ao nthawi zonse; koma mkwiyo wafika pa iwo kufikira chimaliziro.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa