Nagona Asa ndi makolo ake, naikidwa kwa makolo ake m'mzinda wa Davide kholo lake; ndipo Yehosafati mwana wake analowa ufumu m'malo mwake.
Mateyu 1:8 - Buku Lopatulika ndi Asa anabala Yehosafati; ndi Yehosafati anabala Yoramu; ndi Yoramu anabala Uziya; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi Asa anabala Yehosafati; ndi Yehosafati anabala Yoramu; ndi Yoramu anabala Uziya; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Asa adabereka Yehosafati, Yehosafati adabereka Yoramu, Yoramu adabereka Uziya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Asa anabereka Yehosafati, Yehosafati anabereka Yoramu, Yoramu anabereka Uziya. |
Nagona Asa ndi makolo ake, naikidwa kwa makolo ake m'mzinda wa Davide kholo lake; ndipo Yehosafati mwana wake analowa ufumu m'malo mwake.
Ndipo anthu onse a Yuda anatenga Azariya, (ndiye Uziya), ndiye wa zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi, namlonga ufumu m'malo mwa atate wake Amaziya.
Ndipo Yehoramu mwana wa Ahabu analowa ufumu wa Israele mu Samariya m'chaka chakhumi mphambu zisanu ndi zitatu cha Yehosafati mfumu ya Yuda, nakhala mfumu zaka khumi ndi ziwiri.
Ndipo chaka chachisanu cha Yoramu mwana wa Ahabu mfumu ya Israele, pokhala Yehosafati mfumu ya Yuda, Yehoramu mwana wa Yehosafati analowa ufumu.
Ndipo Yehosafati anagona pamodzi ndi makolo ake, naikidwa pamodzi ndi makolo ake m'mzinda wa Davide; ndi Yehoramu mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.