Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 8:16 - Buku Lopatulika

16 Ndipo chaka chachisanu cha Yoramu mwana wa Ahabu mfumu ya Israele, pokhala Yehosafati mfumu ya Yuda, Yehoramu mwana wa Yehosafati analowa ufumu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndipo chaka chachisanu cha Yoramu mwana wa Ahabu mfumu ya Israele, pokhala Yehosafati mfumu ya Yuda, Yehoramu mwana wa Yehosafati analowa ufumu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Chaka chachisanu cha ufumu wa Yoramu, mwana wa Ahabu mfumu ya ku Israele, Yehoramu, mwana wa Yehosafati mfumu ya ku Yuda, adayambapo kulamulira dziko la Yuda.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Chaka chachisanu cha ufumu wa Yoramu mwana wa Ahabu mfumu ya ku Israeli, Yehosafati ali mfumu ya ku Yuda, Yehoramu mwana wake anakhala mfumu ya Ayuda.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 8:16
10 Mawu Ofanana  

Yehosafati anali wa zaka makumi atatu mphambu zisanu, pamene analowa ufumu, nakhala mfumu zaka makumi awiri mphambu zisanu mu Yerusalemu. Ndi dzina la amake linali Azuba mwana wa Sili.


Ndipo Yehosafati anachitana mtendere ndi mfumu ya Israele.


Ndipo Yehosafati anagona ndi makolo ake, naikidwa ndi makolo ake m'mzinda wa Davide kholo lake; ndipo Yehoramu mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.


Ahaziya mwana wa Ahabu anayamba kukhala mfumu ya Israele pa Samariya m'chaka chakhumi mphambu zisanu ndi ziwiri cha Yehosafati mfumu ya Yuda; nakhala mfumu ya Israele zaka ziwiri.


Motero anafa monga mwa mau a Yehova adanena Eliyawo. Ndipo Yehoramu analowa ufumu m'malo mwake chaka chachiwiri cha Yehoramu mwana wa Yehosafati mfumu ya Yuda, pakuti analibe mwana wamwamuna.


Koma Yehoseba mwana wa mfumu Yoramu, mlongo wake wa Ahaziya, anatenga Yowasi mwana wa Ahaziya, namuba pakati pa ana a mfumu akuti aphedwe, iye ndi mlezi, nawaika m'chipinda chogonamo; nambisira Ataliya, ndipo sanaphedwe.


Ndipo Yehoramu mwana wa Ahabu analowa ufumu wa Israele mu Samariya m'chaka chakhumi mphambu zisanu ndi zitatu cha Yehosafati mfumu ya Yuda, nakhala mfumu zaka khumi ndi ziwiri.


Chaka chakhumi ndi ziwiri cha Yoramu mwana wa Ahabu mfumu Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda analowa ufumu wake.


Ndipo okhala mu Yerusalemu anamlonga Ahaziya mwana wake wamng'ono akhale mfumu m'malo mwake; pakuti gulu la anthu, adadzawo pamodzi ndi Aarabu kuchigono, adapha ana oyamba onse. Momwemo Ahaziya mwana wa Yehoramu anakhala mfumu ya Yuda.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa