Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mbiri 3:11 - Buku Lopatulika

11 Yoramu mwana wake, Ahaziya mwana wake, Yowasi mwana wake,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Yoramu mwana wake, Ahaziya mwana wake, Yowasi mwana wake,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Yehosafati adabereka Yoramu. Yoramu adabereka Ahaziya, Ahaziya adabereka Yowasi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Yehosafati anabereka Yehoramu, Yehoramu anabereka Ahaziya, Ahaziya anabereka Yowasi,

Onani mutuwo Koperani




1 Mbiri 3:11
15 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehosafati anagona ndi makolo ake, naikidwa ndi makolo ake m'mzinda wa Davide kholo lake; ndipo Yehoramu mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.


Ahaziya mwana wa Ahabu anayamba kukhala mfumu ya Israele pa Samariya m'chaka chakhumi mphambu zisanu ndi ziwiri cha Yehosafati mfumu ya Yuda; nakhala mfumu ya Israele zaka ziwiri.


Koma Yehoseba mwana wa mfumu Yoramu, mlongo wake wa Ahaziya, anatenga Yowasi mwana wa Ahaziya, namuba pakati pa ana a mfumu akuti aphedwe, iye ndi mlezi, nawaika m'chipinda chogonamo; nambisira Ataliya, ndipo sanaphedwe.


Yowasi anali wa zaka zisanu ndi ziwiri polowa iye ufumu.


Chaka chachisanu ndi chiwiri cha Yehu, Yowasi analowa ufumu wake; nakhala mfumu mu Yerusalemu zaka makumi anai; ndi dzina la mai wake ndiye Zibiya wa ku Beereseba.


Ndipo chaka chachisanu cha Yoramu mwana wa Ahabu mfumu ya Israele, pokhala Yehosafati mfumu ya Yuda, Yehoramu mwana wa Yehosafati analowa ufumu.


Nagona Yoramu ndi makolo ake, naikidwa pamodzi ndi makolo ake m'mzinda wa Davide; ndipo Ahaziya mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.


Chaka chakhumi ndi ziwiri cha Yoramu mwana wa Ahabu mfumu Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda analowa ufumu wake.


Ndipo mwana wa Solomoni ndiye Rehobowamu, Abiya mwana wake, Asa mwana wake, Yehosafati mwana wake,


Amaziya mwana wake, Azariya mwana wake, Yotamu mwana wake,


Ndipo Yehosafati anagona pamodzi ndi makolo ake, naikidwa pamodzi ndi makolo ake m'mzinda wa Davide; ndi Yehoramu mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.


ndiwo anakwerera Yuda, nathyolamo, nalanda chuma chonse chinapezeka m'nyumba ya mfumu, ndi ana ake omwe, ndi akazi ake, osamsiyira mwana, koma Ahaziya yekha mwana wake wamng'ono.


Nabwerera iye kuti amchize ku Yezireele, apole mabala amene adamkantha ku Rama, pamene anayambana ndi Hazaele mfumu ya Aramu. Ndipo Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda anatsikira kukaona Yehoramu mwana wa Ahabu mu Yezireele, popeza anadwala.


Yowasi anali wa zaka zisanu ndi ziwiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu zaka makumi anai; ndi dzina la make ndiye Zibiya wa ku Beereseba.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa