Mateyu 1:5 - Buku Lopatulika ndi Salimoni anabala Bowazi mwa Rahabu; ndi Bowazi anabala Obede mwa Rute; ndi Obede anabala Yese; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi Salimoni anabala Bowazi mwa Rahabu; ndi Bowazi anabala Obede mwa Rute; ndi Obede anabala Yese; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Salimoni adabereka Bowazi mwa Rahabu, Bowazi adabereka Obede mwa Rute, Obede adabereka Yese, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Salimoni anabereka Bowazi amene amayi ake anali Rahabe, Bowazi anabereka Obedi amene amayi ake anali Rute, Obedi anabereka Yese. |
Ndi chikhulupiriro Rahabu wadama uja sanaonongeke pamodzi ndi osamverawo, popeza analandira ozonda ndi mtendere.
Ndipo momwemonso sanayesedwe wolungama Rahabu mkazi wa damayo ndi ntchito kodi, popeza adalandira amithenga, nawatulutsa adzere njira ina?
Momwemo anabwera Naomi ndi Rute Mmowabu mpongozi wake pamodzi naye, amene anabwera kuchokera ku dziko la Mowabu; ndipo anafika ku Betelehemu, pakuyamba anthu kucheka barele.
Nadzitengera iwo akazi a ku Mowabu; wina dzina lake ndiye Oripa, mnzake dzina lake ndiye Rute; ndipo anagonera komweko ngati zaka khumi.