M'dziko momwemo iye anatuluka kunka ku Asiriya, namanga Ninive, ndi mzinda wa Rehoboti, ndi Kala,
Masalimo 83:8 - Buku Lopatulika Asiriya anaphatikana nao; anakhala dzanja la ana a Loti. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Asiriya anaphatikana nao; anakhala dzanja la ana a Loti. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Aasiriya nawonso agwirizana nawo, kuti alimbikitse mphamvu za ana a Loti. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngakhalenso Aasiriya aphatikizana nawo kupereka mphamvu kwa ana a Loti. Sela |
M'dziko momwemo iye anatuluka kunka ku Asiriya, namanga Ninive, ndi mzinda wa Rehoboti, ndi Kala,
Ndipo Yokisani anabala Sheba, ndi Dedani. Ana a Dedani ndi Aasuri, ndi Aletusi, ndi Aleumi.
Pamenepo Pulo mfumu ya Asiriya anadza kudzamenyana ndi dziko, koma Menahemu anampatsa Pulo matalente a siliva chikwi chimodzi; kuti dzanja lake likhale naye kukhazikitsa ufumu m'dzanja lake.
Inu Yehova, mutikomere ife mtima; ife talindira Inu; mukhale dzanja lathu m'mawa ndi m'mawa, chipulumutso chathunso m'nthawi ya mavuto.
Akulu a ku Gebala ndi eni luso ake anali mwa iwe kukonza ziboo zako; zombo zonse za kunyanja pamodzi ndi amalinyero ao anali mwa iwe kusinthana nawe malonda.
Ndipo Yehova anati kwa ine, Usavuta Mowabu, kapena kuutsana naye nkhondo; popeza sindidzakupatsako dziko lake likhale lakolako; pakuti ndinapatsa ana a Loti Ari likhale laolao.