tapenyani, m'mene atibwezera, kudzatiinga m'cholowa chanu, chimene munatipatsa chikhale cholowa chathu.
Masalimo 83:12 - Buku Lopatulika amene anati, Tilande malo okhalamo Mulungu, akhale athu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 amene anati, Tilande malo okhalamo Mulungu, akhale athu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa amene adati, “Tiyeni tilande dziko la Mulungu likhale lathu.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero amene anati, “Tiyeni tilande dziko la msipu la Mulungu.” |
tapenyani, m'mene atibwezera, kudzatiinga m'cholowa chanu, chimene munatipatsa chikhale cholowa chathu.
Amati, Tiyeni tiwaononge asakhalenso mtundu wa anthu; ndipo dzina la Israele lisakumbukikenso.
Ndipo anagwira akalonga awiri a Midiyani, Orebu ndi Zeebu; namupha Orebu ku thanthwe la Orebu; ndi Zeebu anamupha ku choponderamo mphesa cha Zeebu, nalondola Amidiyani; ndipo anadza nayo mitu ya Orebu ndi Zeebu kwa Gideoni tsidya lija la Yordani.
Pamenepo Zeba ndi Zalimuna anati, Tauka iwe mwini nutigwere; pakuti monga munthu momwemo mphamvu yake. Ndipo Gideoni anauka nawapha Zeba ndi Zalimuna, nalanda mphande zinali kukhosi kwa ngamira zao.