Tsiku lonse chimpepulo changa chikhala pamaso panga, ndipo manyazi a pankhope panga andikuta.
Masalimo 69:7 - Buku Lopatulika Pakuti ndalola chotonza chifukwa cha Inu, chimpepulo chakuta nkhope yanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti ndalola chotonza chifukwa cha Inu, chimpepulo chakuta nkhope yanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pakuti ndanyozedwa, nkhope yanga yagwidwa ndi manyazi chifukwa cha Inu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti ndimapirira kunyozedwa chifukwa cha Inu, ndipo manyazi amaphimba nkhope yanga. |
Tsiku lonse chimpepulo changa chikhala pamaso panga, ndipo manyazi a pankhope panga andikuta.
Ndinapereka msana wanga kwa omenya, ndi masaya anga kwa iwo amene anakudzula tsitsi langa; sindinabisire nkhope yanga manyazi ndi kulavulidwa.
Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu; munthu wazisoni, ndi wodziwa zowawa; ndipo ananyozedwa monga munthu wombisira anthu nkhope zao; ndipo ife sitinamlemekeze.
Inu Yehova, mudziwa; mundikumbukire ine, mundiyang'anire Ine, mundibwezere chilango pa ondisautsa ine; musandichotse m'chipiriro chanu; dziwani kuti chifukwa cha Inu ndanyozedwa.
Ndipo Herode ndi asilikali ake anampeputsa Iye, namnyoza, namveka Iye chofunda chonyezimira, nambwezera kwa Pilato.
Yesu, ameneyo, chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala padzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.