Masalimo 51:9 - Buku Lopatulika Muzibisire nkhope yanu zolakwa zanga, ndipo mufafanize mphulupulu zanga zonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Muzibisire nkhope yanu zolakwa zanga, ndipo mufafanize mphulupulu zanga zonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mufulatire machimo anga, mufafanize zoipa zanga zonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mufulatire machimo anga ndi kufafaniza zolakwa zanga zonse. |
Mundichitire ine chifundo, Mulungu, monga mwa kukoma mtima kwanu; monga mwa unyinji wa nsoni zanu zokoma mufafanize machimo anga.
Tiyeni, tsono, tiweruzane, ati Yehova; ngakhale zoipa zanu zili zofiira, zidzayera ngati matalala; ngakhale zili zofiira ngati kapezi, zidzakhala ngati ubweya wa nkhosa, woti mbuu.
Taonani, ndinali ndi zowawa zazikulu, chifukwa cha mtendere wanga; Koma Inu mokonda moyo wanga, munaupulumutsa m'dzanja la chivundi, Pakuti mwaponya m'mbuyo mwanu machimo anga onse.
Pakuti maso anga ali panjira zao zonse, sabisika pa nkhope yanga, mphulupulu yao siibisika pamaso panga.
Ndipo ndidzakuwazani madzi oyera, ndipo mudzakhala oyera; ndidzakuyeretsani kukuchotserani zodetsa zanu zonse, ndi mafano anu nonse.
ndi munthu woyera atenge hisope, namviike m'madzimo, ndi kuwawaza pahema ndi pa zotengera zonse, ndi pa anthu anali pomwepo, ndi pa iye wakukhudza fupa, kapena wophedwa, kapena wakufa, kapena manda.
adatha kutifafanizira cha pa ifecho cholembedwa m'zoikikazo, chimene chinali chotsutsana nafe: ndipo anachichotsera pakatipo, ndi kuchikhomera ichi pamtanda;