Akolose 2:14 - Buku Lopatulika14 adatha kutifafanizira cha pa ifecho cholembedwa m'zoikikazo, chimene chinali chotsutsana nafe: ndipo anachichotsera pakatipo, ndi kuchikhomera ichi pamtanda; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201414 adatha kutifafanizira cha pa ifecho cholembedwa m'zoikikazo, chimene chinali chotsutsana nafe: ndipo anachichotsera pakatipo, ndi kuchikhomera ichi pamtanda; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa14 Adafafaniza kalata ya ngongole yathu, yonena za Malamulo a Mose. Kalatayo inali yotizenga mlandu, koma Iye adaichotsa pakuikhomera pa mtanda. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero14 Anafafaniza kalata ya ngongole yathu, pomwe panali milandu yotitsutsa ife. Iye anayichotsa, nayikhomera pa mtanda. Onani mutuwo |
Pamenepo anaitana alembi a mfumu mwezi woyamba, tsiku lake lakhumi ndi chitatu, nalembera monga mwa zonse Hamani analamulira akazembe ndi ziwanga zoyang'anira maiko ali onse, ndi akalonga a mitundu iliyonse ya anthu, maiko ali onse monga mwa chilembedwe chao, ndi mitundu iliyonse ya anthu monga mwa chinenedwe chao; anazilemba m'dzina la mfumu Ahasuwero, nazisindikiza ndi mphete ya mfumu.