Ndipo ngati nditi, Sindidzamtchula Iye, sindidzanenanso m'dzina lake, pamenepo m'mtima mwanga muli ngati moto wotentha wotsekedwa m'mafupa anga, ndipo ndalema ndi kupirira, sindingathe kupiriranso.
Masalimo 39:3 - Buku Lopatulika Mtima wanga unatentha m'kati mwa ine; unayaka moto pakulingirira ine. Pamenepo ndinalankhula ndi lilime langa, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mtima wanga unatentha m'kati mwa ine; unayaka moto pakulingirira ine. Pamenepo ndinalankhula ndi lilime langa, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mtima wanga udavutika, ndipo pamene ndidasinkhasinkha, mtima wanga udangoyaka moto. Pompo ndidalankhula ndi mau akuti, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mtima wanga unatentha mʼkati mwanga, ndipo pamene ndinkalingalira, moto unayaka; kenaka ndinayankhula ndi lilime langa: |
Ndipo ngati nditi, Sindidzamtchula Iye, sindidzanenanso m'dzina lake, pamenepo m'mtima mwanga muli ngati moto wotentha wotsekedwa m'mafupa anga, ndipo ndalema ndi kupirira, sindingathe kupiriranso.
M'mwemo mzimu unandinyamula ndi kuchoka nane; ndipo ndinamuka wowawidwa, womyuka mtima; koma dzanja la Yehova linandigwirizitsa.
Ndipo anati wina kwa mnzake, Mtima wathu sunali wotentha m'kati mwathu nanga m'mene analankhula nafe m'njira, m'mene anatitsegulira malembo?