Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 20:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo ngati nditi, Sindidzamtchula Iye, sindidzanenanso m'dzina lake, pamenepo m'mtima mwanga muli ngati moto wotentha wotsekedwa m'mafupa anga, ndipo ndalema ndi kupirira, sindingathe kupiriranso.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo ngati nditi, Sindidzamtchula Iye, sindidzanenanso m'dzina lake, pamenepo m'mtima mwanga muli ngati moto wotentha wotsekedwa m'mafupa anga, ndipo ndalema ndi kupirira, sindingathe kupiriranso.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Ndikanena kuti, “Sindidzalalikanso za Chauta, sindidzalankhulanso m'dzina lake,” mau anu, Inu Chauta, amayaka ngati moto mumtima mwanga. Ndimayesa kuŵasunga m'kati, koma pambuyo pake ndimaŵatulutsa popeza kuti sindingathe kupirira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Koma ndikanena kuti, “Sindidzalalikiranso za Iye kapena kuyankhulanso mʼdzina lake,” mawu anu amayaka ngati moto mu mtima mwanga, amakhaladi ngati moto wotsekeredwa mʼmafupa anga. Ndapirira kusunga mawu anu mu mtima mwanga osawatulutsa, koma sindingathe kupirirabe.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 20:9
21 Mawu Ofanana  

Mtima wanga unatentha m'kati mwa ine; unayaka moto pakulingirira ine. Pamenepo ndinalankhula ndi lilime langa,


Kodi mau anga safanafana ndi moto? Ati Yehova, ndi kufanafana ndi nyundo imene iphwanya mwala?


Za aneneri. Mtima wanga usweka m'kati mwanga, mafupa anga onse anthunthumira; ndinga munthu woledzera, ngati munthu amene vinyo anamposa; chifukwa cha Yehova, ndi chifukwa cha mau ake opatulika.


Matumbo anga, matumbo anga! Ndipoteka pamtima panga penipeni; mtima wanga sukhala pansi m'kati mwanga; sindithai kutonthola; pakuti wamva, moyo wanga, mau a lipenga, mbiri ya nkhondo.


Chifukwa chake ndadzala ndi ukali wa Yehova; ndalema ndi kudzikaniza; tsanulirani pa ana a pabwalo, ndi pa misonkhano ya anyamata, pakuti ngakhale mwamuna ndi mkazi wake adzatengedwa, okalamba ndi iye amene achuluka masiku ake.


M'mwemo mzimu unandinyamula ndi kuchoka nane; ndipo ndinamuka wowawidwa, womyuka mtima; koma dzanja la Yehova linandigwirizitsa.


Nati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, dyetsa m'mimba mwako, nudzaze matumbo ako ndi mpukutu uwu ndakupatsawu. M'mwemo ndinaudya, ndi m'kamwa mwanga munazuna ngati uchi.


Mkango ukabangula, ndani amene saopa? Ambuye Yehova wanena, ndani amene sanenera?


Nyamuka, pita ku Ninive, mzinda waukuluwo, nulalikire motsutsana nao; pakuti choipa chao chandikwerera pamaso panga.


Koma Yona ananyamuka kuti athawire ku Tarisisi, kuzemba Yehova; ndipo anatsikira ku Yopa, napezako chombo chomuka ku Tarisisi, napereka ndalama zake, natsikira m'menemo, kuti apite nao ku Tarisisi kuzemba Yehova.


Koma Yesu anati kwa iye, Palibe munthu wakugwira chikhasu, nayang'ana za kumbuyo, ayenera Ufumu wa Mulungu.


Pamene Paulo analindira iwo pa Atene, anavutidwa mtima pamene anaona mzinda wonse wadzala ndi mafano.


Koma pamene Silasi ndi Timoteo anadza potsika ku Masedoniya, Paulo anapsinjidwa ndi mau, nachitira umboni kwa Ayuda kuti Yesu ndiye Khristu.


pakuti sitingathe ife kuleka kulankhula zimene tinaziona ndi kuzimva.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa