ndipo ndinati, Mulungu wanga, ndigwa nkhope, ndi kuchita manyazi kuweramutsa nkhope yanga kwa inu Mulungu wanga, popeza mphulupulu zathu zachuluka pamutu pathu, ndi kupalamula kwathu kwakula kufikira mu Mwamba.
Masalimo 38:4 - Buku Lopatulika Pakuti mphulupulu zanga zapitirira pamutu panga; ndathodwa nazo monga ndi katundu wolemera. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti mphulupulu zanga zapitirira pamutu panga; ndathodwa nazo monga ndi katundu wolemera. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Machimo anga andimiza msinkhu, akundilemera ngati katundu woposa mphamvu zanga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kulakwa kwanga kwandipsinja ngati katundu wolemera kwambiri kuposa mphamvu zanga. |
ndipo ndinati, Mulungu wanga, ndigwa nkhope, ndi kuchita manyazi kuweramutsa nkhope yanga kwa inu Mulungu wanga, popeza mphulupulu zathu zachuluka pamutu pathu, ndi kupalamula kwathu kwakula kufikira mu Mwamba.
Pakuti zoipa zosawerengeka zandizinga, zochimwa zanga zandipeza kotero kuti sindikhoza kupenya; ziposa tsitsi la mutu wanga, ndipo wandichokera mtima.
Iye adzaona zotsatira mavuto a moyo wake, nadzakhuta nazo; ndi nzeru zake mtumiki wanga wolungama adzalungamitsa ambiri, nadzanyamula mphulupulu zao.
Goli la zolakwa zanga lamangidwa ndi dzanja lake; zalukidwa, zakwera pakhosi panga; iye wakhumudwitsa mphamvu yanga; Ambuye wandipereka m'manja mwao, sindithai kuwagonjetsa.
Ndipo akadyako nyama ya nsembe zoyamika zake tsiku lachitatu, sikuvomerezeka kumene; sadzamwerengera wobwera nayo; ndiyo chinthu chonyansa, ndipo munthu wakudyako adzasenza mphulupulu zake.
amene anasenza machimo athu mwini yekha m'thupi mwake pamtanda, kuti ife, titafa kumachimo, tikakhale ndi moyo kutsata chilungamo; ameneyo mikwingwirima yake munachiritsidwa nayo.