Masalimo 22:4 - Buku Lopatulika Makolo athu anakhulupirira Inu; anakhulupirira, ndipo munawalanditsa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Makolo athu anakhulupirira Inu; anakhulupirira, ndipo munawalanditsa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Makolo athu ankadalira Inu. Zoonadi, ankakhulupirira Inu, ndipo Inu munkaŵapulumutsa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa inu makolo athu anadalira; iwo anadalira ndipo Inu munawapulumutsa. |
Ndipo anati, Dzina lako silidzatchedwanso Yakobo, koma Israele, chifukwa unayesana naye Mulungu ndithu, ndipo unapambana.
Ndipo kunali, pakuchita limodzi amalipenga ndi oimba, kumveketsa mau amodzi akulemekeza ndi kuyamika Yehova, ndi pakukweza mau ao pamodzi ndi malipenga, ndi nsanje, ndi zoimbira zina, ndi kulemekeza Yehova, ndi kuti, Pakuti Iye ndiye wabwino, pakuti chifundo chake chikhala chikhalire; pamenepo mtambo unadzaza nyumbayi, ndiyo nyumba ya Yehova;
Ndipo Israele anaiona ntchito yaikulu imene Yehova anachitira Aejipito, ndipo anthuwo anaopa Yehova; nakhulupirira Yehova ndi mtumiki wake Mose.