Mulungu ndipo adalenga zinsomba zazikulu ndi zoyendayenda zamoyo zakuchuluka m'madzi mwa mitundu yao, ndi mbalame zamapiko, yonse monga mwa mtundu wake: ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino.
Masalimo 148:7 - Buku Lopatulika Lemekezani Yehova kochokera ku dziko lapansi, zinsomba inu, ndi malo ozama onse; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Lemekezani Yehova kochokera ku dziko lapansi, zinsomba inu, ndi malo ozama onse; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tamandani Chauta inu okhala pa dziko lapansi, inu zilombo za m'madzi ndi nyanja zonse zozama, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tamandani Yehova pa dziko lapansi, inu zolengedwa zikuluzikulu za mʼnyanja, ndi nyanja zonse zakuya, |
Mulungu ndipo adalenga zinsomba zazikulu ndi zoyendayenda zamoyo zakuchuluka m'madzi mwa mitundu yao, ndi mbalame zamapiko, yonse monga mwa mtundu wake: ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino.
Namuka iye, napeza mtembo wake wogwera m'njira, ndi bulu ndi mkango zili chiimire pafupi ndi mtembo. Mkango udalibe kudya mtembo, kapena kukadzula bulu.
Ntchito zanu zichulukadi, Yehova! Munazichita zonse mwanzeru; dziko lapansi lidzala nacho chuma chanu.
Tsiku limenelo Yehova ndi lupanga lake lolimba ndi lalikulu ndi lamphamvu adzalanga Leviyatani njoka yothamanga, ndi Leviyatani njoka yopindikapindika; nadzapha ching'ona chimene chili m'nyanja.
Nyama za m'thengo zidzandilimekeza, ankhandwe ndi nthiwatiwa; chifukwa ndipatsa madzi m'chipululu, ndi mitsinje m'mkhwangwala, ndimwetse anthu anga osankhika;