Kwa Inu, Yehova, ndidzafuulira; thanthwe langa, musandikhalire ngati wosamva; pakuti ngati munditontholera ine, ndidzafanana nao iwo akutsikira kumanda.
Masalimo 142:2 - Buku Lopatulika Nditsanulira kudandaula kwanga pamaso pake; ndionetsa msauko wanga pamaso pake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nditsanulira kudandaula kwanga pamaso pake; ndionetsa msauko wanga pamaso pake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndikupereka madandaulo anga kwa Iye, ndikutchula mavuto anga pamaso pake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndikukhuthula madandawulo anga pamaso pake; ndikufotokoza za masautso anga pamaso pake. |
Kwa Inu, Yehova, ndidzafuulira; thanthwe langa, musandikhalire ngati wosamva; pakuti ngati munditontholera ine, ndidzafanana nao iwo akutsikira kumanda.
Ndidzikumbukira izi ndipo nditsanulira moyo wanga m'kati mwa ine, pakuti ndinkapita ndi unyinji wa anthu, ndinawatsogolera kunyumba ya Mulungu, ndi mau akuimbitsa ndi kuyamika, ndi unyinji wakusunga dzuwa lokondwera.
Khulupirirani pa Iye nyengo zonse, anthu inu, tsanulirani mitima yanu pamaso pake. Mulungu ndiye pothawirapo ife.
Ndipo momwemonso Mzimu athandiza kufooka kwathu; pakuti chimene tizipempha monga chiyenera, sitidziwa; koma Mzimu mwini atipempherera ndi zobuula zosatheka kuneneka;
Ameneyo, m'masiku a thupi lake anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kumpulumutsa Iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu,