Masalimo 139:12 - Buku Lopatulika Ungakhale mdima sudetsa pamaso panu, koma usiku uwala ngati usana; mdima ukunga kuunika. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ungakhale mdima sudetsa pamaso panu, koma usiku uwala ngati usana; mdima ukunga kuunika. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa ngakhale mdimawo, kwa Inu si mdima konse, kwa Inu usiku umaŵala ngati usana, mdima uli ngati kuŵala. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero komabe mdimawo sudzakhala mdima kwa Inu; usiku udzawala ngati masana, pakuti mdima uli ngati kuwunika kwa Inu. |
nulowa pakati pa ulendo wa Aejipito ndi ulendo wa Aisraele; ndipo mtambo unachita mdima, komanso unaunikira usiku; ndipo ulendo wina sunayandikizane ndi unzake usiku wonse.
Iye avumbulutsa zinthu zakuya ndi zinsinsi; adziwa zokhala mumdima, ndi kuunika kumakhala kwa Iye.
Ndipo palibe cholembedwa chosaonekera pamaso pake, koma zonse zikhala za pambalambanda ndi zovundukuka pamaso pake pa Iye amene tichita naye.