Munawapatsanso maufumu, ndi mitundu ya anthu, nimunawagawa m'madera, motero analandira likhale laolao dziko la Sihoni, ndilo dziko la mfumu ya ku Hesiboni, ndi dziko la Ogi mfumu ya ku Basani.
Masalimo 135:11 - Buku Lopatulika Sihoni mfumu ya Aamori, ndi Ogi mfumu ya Basani, ndi maufumu onse a Kanani: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Sihoni mfumu ya Aamori, ndi Ogi mfumu ya Basani, ndi maufumu onse a Kanani: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Sihoni, mfumu ya Aamori, ndi Ogi, mfumu ya ku Basani, pamodzi ndi maufumu onse a ku Kanani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Sihoni mfumu ya Aamori, Ogi mfumu ya Basani, ndi maufumu onse a ku Kanaani; |
Munawapatsanso maufumu, ndi mitundu ya anthu, nimunawagawa m'madera, motero analandira likhale laolao dziko la Sihoni, ndilo dziko la mfumu ya ku Hesiboni, ndi dziko la Ogi mfumu ya ku Basani.
Koma Sihoni mfumu ya Hesiboni sanatilole kupitira kwao; popeza Yehova Mulungu wanu anaumitsa mzimu wake, nalimbitsa mtima wake, kuti ampereke m'dzanja lanu, monga lero lino.
Ndipo pamene munafika pamalo pano, Sihoni mfumu ya Hesiboni, ndi Ogi mfumu ya Basani, anatuluka kudzakomana nafe kunkhondo, ndipo tinawakantha;
Ndipo ndinatuma mavu atsogolere inu, amene anawaingitsa pamaso panu, ndiwo mafumu awiri a Aamori; osati ndi lupanga lako, kapena ndi uta wako ai.