Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Masalimo 118:9 - Buku Lopatulika

Kuthawira kwa Yehova nkokoma koposa kukhulupirira akulu.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Kuthawira kwa Yehova nkokoma koposa kukhulupirira akulu.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kuthaŵira kwa Chauta nkwabwino kupambana kukhulupirira mafumu.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Nʼkwabwino kuthawira kwa Yehova kusiyana ndi kudalira mafumu.

Onani mutuwo



Masalimo 118:9
8 Mawu Ofanana  

Tsoka kwa iwo amene atsikira kunka ku Ejipito kukathandizidwa, natama akavalo; nakhulupirira magaleta, pakuti ali ambiri, ndi okwera pa akavalo, pakuti ali a mphamvu zambiri; koma sayang'ana Woyera wa Israele, ngakhale kumfuna Yehova!


Pamenepo Asiriya adzagwa ndi lupanga losati la munthu; ndi lupanga losati la anthu lidzammaliza iye; ndipo iye adzathawa lupanga, ndi anyamata ake adzalamba.


Muja anakugwira ndi dzanja unathyoka, ndi kulasa mapewa ao onse; ndi muja anakutsamira unathyoka, ndi kuwagwedeza ziuno zao zonse.


Pakuti tsopano adzati, Tilibe mfumu, popeza sitiopa Yehova; ndi mfumu idzatichitira chiyani?