Anene tsono Israele, kuti chifundo chake nchosatha.
Aisraele anene kuti, “Chikondi chake nchamuyaya.”
Israeli anene kuti: “Chikondi chake ndi chosatha.”
Ntchito zanu zonse zidzakuyamikani, Yehova; ndi okondedwa anu adzakulemekezani.
Ndipo onse amene atsata chilangizo ichi, mtendere ndi chifundo zikhale pa iwo, ndi pa Israele wa Mulungu.
Potero mwa Iye tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.