Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Marko 1:5 - Buku Lopatulika

Ndipo anatuluka a ku dziko lonse la Yudeya, ndi a ku Yerusalemu onse; nadza kwa iye nabatizidwa ndi iye mumtsinje Yordani, powulula machimo ao.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo anatuluka a ku dziko lonse la Yudeya, ndi a ku Yerusalemu onse; nadza kwa iye nabatizidwa ndi iye mumtsinje Yordani, powulula machimo ao.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Anthu ochokera ku dera lonse la Yudeya ndi a ku Yerusalemu ankadza kwa iye. Tsono ankati iwo akaulula machimo ao, iye nkumaŵabatiza mu Mtsinje wa Yordani.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Madera onse a ku Yudeya ndi anthu onse a ku Yerusalemu anatuluka napita kwa iye. Akavomereza machimo awo, amawabatiza mu mtsinje wa Yorodani.

Onani mutuwo



Marko 1:5
15 Mawu Ofanana  

Ndinavomera choipa changa kwa Inu; ndipo mphulupulu yanga sindinaibise. Ndinati, Ndidzaululira Yehova machimo anga; ndipo munakhululukira choipa cha kulakwa kwanga.


Wobisa machimo ake sadzaona mwai; koma wakuwavomereza, nawasiya adzachitidwa chifundo.


Ndipo inamtsata mipingomipingo ya anthu ochokera ku Galileya, ndi ku Dekapoli ndi ku Yerusalemu, ndi ku Yudeya, ndi ku tsidya lija la Yordani.


Yohane anadza nabatiza m'chipululu, nalalikira ubatizo wa kutembenuka mtima wakuloza ku chikhululukiro cha machimo.


Ndipo Yohane anavala ubweya wa ngamira, ndi lamba lachikopa m'chuuno mwake, nadya dzombe ndi uchi wakuthengo.


Zinthu izi zinachitika mu Betaniya tsidya lija la Yordani, pomwe analikubatiza Yohane.


Ndipo Yohane analinkubatiza mu Ainoni pafupi pa Salimu, chifukwa panali madzi ambiri pamenepo; ndipo analinkufikako anthu, nalinkubatizidwa.


Iyeyo anali nyali yoyaka ndi yowala; ndipo inu munafuna kukondwera m'kuunika kwake kanthawi.


Ndipo ambiri a iwo akukhulupirirawo anadza, navomereza, nafotokoza machitidwe ao.


Koma Petro anati kwa iwo, Lapani, batizidwani yense wa inu m'dzina la Yesu Khristu kuloza ku chikhululukiro cha machimo anu; ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.


Chifukwa chake muvomerezane wina ndi mnzake machimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama likhoza kwakukulu m'machitidwe ake.


Ndipo Yoswa anati kwa Akani, Mwana wanga, uchitiretu ulemu Yehova Mulungu wa Israele, numlemekeze Iye; nundiuze tsopano, wachitanji? Usandibisire.