Ndipo m'mzinda uliwonse, kapena m'mudzi, mukalowamo, mufunsitse amene ali woyenera momwemo; ndipo bakhalani komweko kufikira mutulukamo.
Luka 7:4 - Buku Lopatulika Ndipo iwo, pakufika kwa Yesu, anampempha Iye koumirira, nati, Ayenera iye kuti mumchitire ichi; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iwo, pakufika kwa Yesu, anampempha Iye koumirira, nati, Ayenera iye kuti mumchitire ichi; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene adafika kwa Yesu, adampempha kolimba namuuza kuti, “Ameneyu ngwoyeneradi kuti mumchitire zimenezi, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo atafika kwa Yesu, anamudandaulira kwambiri, nati, “Munthuyu ayenera kuthandizidwa |
Ndipo m'mzinda uliwonse, kapena m'mudzi, mukalowamo, mufunsitse amene ali woyenera momwemo; ndipo bakhalani komweko kufikira mutulukamo.
Ndipo ngati nyumbayo ili yoyenera, mtendere wanu udze pa iyo, koma ngati siili yoyenera, mtendere wanu ubwerere kwa inu.
koma iwo akuyesedwa oyenera kufikira dziko lijalo, ndi kuuka kwa akufa, sakwatira kapena kukwatiwa.
Ndipo pamene iye anamva za Yesu, anatuma kwa Iye akulu a Ayuda, namfunsa Iye kuti adze kupulumutsa kapolo wake.
ndiye munthu wopembedza, ndi wakuopa Mulungu ndi banja lake lonse, amene anapatsa anthu zachifundo zambiri, napemphera Mulungu kosaleka.
Komatu uli nao maina owerengeka mu Sardi, amene sanadetse zovala zao; ndipo adzayenda ndi Ine m'zoyera; chifukwa ali oyenera.