Kuti analowa m'nyumba ya Mulungu, nadya mikate yoonetsa, imene yosaloleka kudya iye kapena amene anali naye, koma ansembe okhaokha.
Luka 6:4 - Buku Lopatulika kuti analowa m'nyumba ya Mulungu, natenga mikate yoonetsera, nadya, napatsanso iwo anali naye pamodzi; imeneyi yosaloledwa kudya ena koma ansembe okha? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 kuti analowa m'nyumba ya Mulungu, natenga mikate yoonetsera, nadya, napatsanso iwo anali naye pamodzi; imeneyi yosaloledwa kudya ena koma ansembe okha? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Suja adaloŵa m'Nyumba ya Mulungu, natenga buledi woperekedwa kwa Mulungu, naadya, nkupatsakonso anzake aja? Chonsecho nkosaloledwa kuti buledi ameneyo wina aliyense nkumudya kupatula ansembe okha.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye analowa mʼnyumba ya Mulungu ndipo atatenga buledi wopatulika anadya amene ndi ololedwa kudya ansembe okha. Ndipo anaperekanso wina kwa anzake.” |
Kuti analowa m'nyumba ya Mulungu, nadya mikate yoonetsa, imene yosaloleka kudya iye kapena amene anali naye, koma ansembe okhaokha.
Chomwecho wansembeyo anampatsa mkate wopatulika, popeza panalibe mkate wina, koma mkate woonekera, umene adauchotsa pamaso pa Yehova, kuti akaike mkate wotentha tsiku lomwelo anachotsa winawo.