Ndipo amisonkho omwe anadza kudzabatizidwa, nati kwa iye, Mphunzitsi, ife tizichita chiyani?
Luka 3:10 - Buku Lopatulika Ndipo anthu a makamu anamfunsa iye, nanena, Ndipo tsono tizichita chiyani? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anthu a makamu anamfunsa iye, nanena, Ndipo tsono tizichita chiyani? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo anthu aja adafunsa Yohane kuti, “Tsono ife tizichita zabwino zanji?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Gulu la anthuwo linafunsa kuti, “Nanga tsono tichite chiyani?” |
Ndipo amisonkho omwe anadza kudzabatizidwa, nati kwa iye, Mphunzitsi, ife tizichita chiyani?
Ndipo asilikali omwe anamfunsa iye, nati, Nanga ife tizichita chiyani? Ndipo iye anati kwa iwo, Musaopse, musanamize munthu aliyense; khalani okhuta ndi kulipira kwanu.
Chifukwa chake balani zipatso zakuyenera kulapa mtima, ndipo musayambe kunena mwa inu nokha, Atate wathu tili naye ndiye Abrahamu: pakuti ndinena kwa inu, kuti ali ndi mphamvu Mulungu, mwa miyala iyi, kuukitsira Abrahamu ana.
Koma pamene anamva ichi, analaswa mtima, natitu kwa Petro ndi atumwi enawo, Tidzachita chiyani, amuna inu, abale?
Koma Petro anati kwa iwo, Lapani, batizidwani yense wa inu m'dzina la Yesu Khristu kuloza ku chikhululukiro cha machimo anu; ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.