Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 16:30 - Buku Lopatulika

30 nawatulutsira iwo kunja, nati, Ambuye, ndichitenji kuti ndipulumuke?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 nawatulutsira iwo kunja, nati, Ambuye, ndichitenji kuti ndipulumuke?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 Tsono adaŵatulutsira kunja, naŵafunsa kuti, “Mabwana, Kodi ndichite chiyani kuti ndipulumuke?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 Iye anawatulutsa kunja ndipo anawafunsa kuti, “Amuna inu, ndichite chiyani kuti ndipulumuke?”

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 16:30
16 Mawu Ofanana  

Potero munthu akhala bwanji wolungama kwa Mulungu? Kapena wobadwa ndi mkazi akhala woyera bwanji?


Chimene sindichiona mundilangize ndi Inu, ngati ndachita chosalungama sindidzabwerezanso.


Kodi kumeneku si kusala kudya kumene ndinakusankha: kumasula nsinga za zoipa, ndi kumasula zomanga goli, ndi kuleka otsenderezedwa amuke mfulu, ndi kuti muthyole magoli onse?


Pamenepo udzaitana, ndipo Yehova adzayankha; udzafuula ndipo Iye adzati, Ndine pano. Ngati uchotsa pakati pa iwe goli, kukodolana moipa, ndi kulankhula moipa,


Onetsani inu zipatso zakuyenera kutembenuka mtima:


Odala ali akuchitira chifundo; chifukwa adzalandira chifundo.


Ndipo anthu a makamu anamfunsa iye, nanena, Ndipo tsono tizichita chiyani?


nafuula nati, Anthuni, bwanji muchita zimenezi? Ifenso tili anthu a mkhalidwe wathu umodzimodzi ndi wanu, akulalikira kwa inu Uthenga Wabwino, wakuti musiye zinthu zachabe izi, nimutembenukire kwa Mulungu wamoyo, amene analenga zakumwamba ndi zapansi, ndi nyanja, ndi zonse zili momwemo:


Ameneyo anatsata Paulo ndi ife, nafuula, kuti, Anthu awa ndi akapolo a Mulungu wa Kumwambamwamba, amene akulalikirani inu njira ya chipulumutso.


Pakumva iye kulamulira kotero anawaika m'chipinda cha m'kati, namangitsa mapazi ao m'zigologolo.


Koma pamene anamva ichi, analaswa mtima, natitu kwa Petro ndi atumwi enawo, Tidzachita chiyani, amuna inu, abale?


Ndipo ndinati, Ndidzachita chiyani, Ambuye? Ndipo Ambuye anati kwa ine, Tauka, pita ku Damasiko; kumeneko adzakufotokozera zonse zoikika kwa iwe uzichite.


komatu, uka, nulowe m'mzinda, ndipo kudzanenedwa kwa iwe chimene uyenera kuchita.


Pakuti chiweruziro chilibe chifundo kwa iye amene sanachite chifundo; chifundo chidzitamandira kutsutsana nacho chiweruziro.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa