Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Luka 2:2 - Buku Lopatulika

ndiko kulembera koyamba pokhala Kwirinio kazembe wa Siriya.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

ndiko kulembera koyamba pokhala Kwirinio kazembe wa Siriya.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kalembera ameneyu anali woyamba, ndipo adachitika pamene Kwirinio anali bwanamkubwa wa dziko la Siriya.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

(Uyu ndi kalembera woyamba amene anachitika pamene Kureniyo anali bwanamkubwa wa Siriya).

Onani mutuwo



Luka 2:2
9 Mawu Ofanana  

Ndipo mbiri yake inabuka ku Siriya konse: ndipo anatengera kwa Iye onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundumitundu, ndi ogwidwa ndi ziwanda, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawachiritsa.


Ndipo kunali masiku aja, kuti lamulo linatuluka kwa Kaisara Augusto kuti dziko lonse lokhalamo anthu lilembedwe;


Ndipo onse anamuka kulembedwa, munthu aliyense kumzinda wake.


Ndipo pa chaka chakhumi ndi chisanu cha ufumu wa Tiberio Kaisara, pokhala Pontio Pilato kazembe wa Yudeya, ndi Herode chiwanga cha Galileya, ndi Filipo mbale wake chiwanga cha dziko la Itureya ndi la Trakoniti, ndi Lisaniasi chiwanga cha Abilene;


ameneyo anali ndi kazembe Sergio Paulo, ndiye munthu wanzeru. Yemweyo anaitana Barnabasi ndi Saulo, nafunitsa kumva mau a Mulungu.


Tsono pamene Galio anali chiwanga cha Akaya, Ayuda ndi mtima umodzi anamuukira Paulo, nanka naye kumpando wachiweruziro,


Klaudio Lisiasi kwa kazembe womveketsa Felikisi, ndikupatsani moni.


Ndipo ananyamuka mfumu, ndi kazembe, ndi Berenise, ndi iwo akukhala nao;


Atapita ameneyo, anauka Yudasi wa ku Galileya, masiku a kalembera, nakopa anthu amtsate. Iyeyunso anaonongeka, ndi onse amene anamvera iye anabalalitsidwa.