Ndipo iye anati Ndileke ndimuke, chifukwa kulinkucha. Ndipo Yakobo anati, Sindidzakuleka iwe kuti umuke, ukapanda kundidalitsa ine.
Luka 11:8 - Buku Lopatulika Ndinena ndi inu, ngakhale sadzauka ndi kumpatsa, chifukwa ali bwenzi lake, koma chifukwa cha liuma lake adzauka nadzampatsa iye zilizonse azisowa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndinena ndi inu, ngakhale sadzauka ndi kumpatsa, chifukwa ali bwenzi lake, koma chifukwa cha liuma lake adzauka nadzampatsa iye zilizonse azisowa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndithu ndikunenetsa kuti adzauka nkumupatsa, osati chifukwa ndi bwenzi lake, koma chifukwa cha khama la wopempha uja. Ndipo adzampatsa zonse zimene akusoŵa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ine ndikukuwuzani kuti adzadzuka ndi kumupatsa bulediyo, osati chifukwa ndi bwenzi lake, koma chifukwa cha liwuma la munthu wopemphayo, ndipo kudzamupatsa zonse zimene akuzifuna. |
Ndipo iye anati Ndileke ndimuke, chifukwa kulinkucha. Ndipo Yakobo anati, Sindidzakuleka iwe kuti umuke, ukapanda kundidalitsa ine.
ndipo iyeyu wa m'katimo poyankha akati, Usandivuta; pakhomo mpotseka tsopano, ndipo ana anga ali nane pamodzi pogona; sindingathe kuuka ndi kukupatsa?
Ndipo ndikudandaulirani, abale, ndi Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi chikondi cha Mzimu, kuti mudzalimbike pamodzi ndi ine m'mapemphero anu kwa Mulungu chifukwa cha ine;
Pakuti ndifuna kuti inu mudziwe nkhawa imene ndili nayo chifukwa cha inu, ndi iwowa a mu Laodikea, ndi onse amene sanaone nkhope yanga m'thupi;
Akupatsani moni Epafra ndiye wa kwa inu, ndiye kapolo wa Khristu Yesu, wakulimbika m'mapemphero ake masiku onse chifukwa cha inu, kuti mukaime amphumphu ndi odzazidwa m'chifuniro chonse cha Mulungu.
Ndipo analira pamaso pake masiku asanu ndi awiriwo pochitika madyerero ao; koma kunali kuti tsiku lachisanu ndi chiwiri anamuuza, popeza anamuumiriza; ndipo anatanthauzira anthu a mtundu wake mwambiwo.
Ndipo panali, m'mene iye analikupempherabe pamaso pa Yehova, Eli anapenyerera pakamwa pake.