Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 11:7 - Buku Lopatulika

7 ndipo iyeyu wa m'katimo poyankha akati, Usandivuta; pakhomo mpotseka tsopano, ndipo ana anga ali nane pamodzi pogona; sindingathe kuuka ndi kukupatsa?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 ndipo iyeyu wa m'katimo poyankha akati, Usandivuta; pakhomo mpotseka tsopano, ndipo ana anga ali nane pamodzi pogona; sindikhoza kuuka ndi kukupatsa?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Koma wam'nyumbayo nkuyankha kuti, ‘Usandivute, ndatseka kale pa khomo, ndipo ine ndi ana anga tagona, sindingadzukenso kuti ndikupatse bulediyo.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 “Ndipo yerekezani kuti amene ali mʼnyumbamo ndi kuyankha kuti, ‘Usandivutitse ine, ndatseka kale chitseko, ndipo ine ndi ana anga tagona. Ine sindingadzukenso kuti ndidzakupatse.’

Onani mutuwo Koperani




Luka 11:7
7 Mawu Ofanana  

Ndinayankha kuti, Ndavula malaya anga, ndiwavalenso bwanji? Ndatsuka mapazi anga; ndiwadetserenji?


Ndipo pamene iwo analikumuka kukagula, mkwati anafika; ndipo okonzekawo analowa naye pamodzi muukwati; ndipo anatseka pakhomo.


popeza wandidzera bwenzi langa lochokera paulendo ndipo ndilibe chompatsa;


Ndinena ndi inu, ngakhale sadzauka ndi kumpatsa, chifukwa ali bwenzi lake, koma chifukwa cha liuma lake adzauka nadzampatsa iye zilizonse azisowa.


Pamene atauka mwini nyumba natseka pakhomo, ndipo inu mudzayamba kuima pabwalo, ndi kugogoda pachitseko, ndi kunena, Ambuye titsegulireni ife; ndipo Iye adzayankha nadzati ndi inu, Sindidziwa inu kumene muchokerako;


Ndipo Yesu anapita nao. Ndipo pakufika Iye tsono pafupi pa nyumba yake, kenturiyo anatuma kwa Iye abwenzi ake, kunena naye, Ambuye, musadzivute; pakuti sindiyenera ine kuti mudzalowe pansi pa tsindwi langa;


Kuyambira tsopano palibe munthu andivute, pakuti ndili nayo ine m'thupi mwanga mikwingwirima ya Yesu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa