Mundichotsere kutali zachabe ndi mabodza; musandipatse umphawi, ngakhale chuma, mundidyetse zakudya zondiyenera;
Luka 11:3 - Buku Lopatulika tipatseni ife tsiku ndi tsiku chakudya cha patsiku. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 tipatseni ife tsiku ndi tsiku chakudya cha patsiku. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mutipatse ife tsiku lililonse chakudya chathu chamasikuwonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mutipatse chakudya chathu chalero, |
Mundichotsere kutali zachabe ndi mabodza; musandipatse umphawi, ngakhale chuma, mundidyetse zakudya zondiyenera;
iye adzakhala pamsanje; malo ake ochinjikiza adzakhala malinga amiyala; chakudya chake chidzapatsidwa kwa iye; madzi ake adzakhala chikhalire.
Chifukwa chake musadere nkhawa za mawa; pakuti mawa adzadzidera nkhawa iwo okha. Zikwanire tsiku zovuta zake.
Amenewa anali mfulu koposa a mu Tesalonika, popeza analandira mau ndi kufunitsa kwa mtima wonse, nasanthula m'malembo masiku onse, ngati zinthu zinali zotero.