Ndipo anaika chakudya pamaso pake: koma anati, Sindidzadya ndisananene chimene ndadzera. Ndipo anati, Nenatu.
Luka 10:4 - Buku Lopatulika Musanyamule thumba la ndalama kapena thumba la kamba, kapena nsapato; nimusalonjere munthu panjira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Musanyamule thumba la ndalama kapena thumba la kamba, kapena nsapato; nimusalonjere munthu panjira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Musatenge chikwama cha ndalama, kapena thumba lapaulendo, kapenanso nsapato zapadera ai. Musaimenso kuti mupereke moni pa njira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Musatenge chikwama kapena thumba kapena nsapato; ndipo musalonjere wina aliyense pa njira. |
Ndipo anaika chakudya pamaso pake: koma anati, Sindidzadya ndisananene chimene ndadzera. Ndipo anati, Nenatu.
Ndipo iye anati kwa iwo, Musandichedwetse ine, pakuti Yehova wandiyendetsa bwino m'njira yanga: mundilole ine ndinke kwa mbuyanga.
Pamenepo anamangirira bulu mbereko, nati kwa mnyamata wake, Kusa, tiye; usandilezetsa kuyendaku, ndikapanda kukuuza.
Pamenepo anati kwa Gehazi, Udzimangire m'chuuno, nutenge ndodo yanga m'dzanja lako, numuke; ukakomana ndi munthu usampatse moni; wina akakupatsa moni usamyankhe; ukaike ndodo yanga pankhope pa mwanayo.
Ndipo anadziitanira khumi ndi awiriwo, nayamba kuwatumiza iwo awiriawiri; nawapatsa mphamvu pa mizimu yonyansa;
Ndipo anati kwa iwo, Pamene ndinakutumizani opanda thumba la ndalama, ndi thumba la kamba, ndi nsapato, munasowa kanthu kodi? Anati iwo, Iai.
Ndipo Davide ananena ndi Ahimeleki, Nanga pano m'dzanja mwanu mulibe mkondo kapena lupanga kodi? Chifukwa ine sindinatenge lupanga langa kapena zida zanga, popeza mlandu wa mfumu ukuti ndifulumire.