Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 4:24 - Buku Lopatulika

24 Pamenepo anamangirira bulu mbereko, nati kwa mnyamata wake, Kusa, tiye; usandilezetsa kuyendaku, ndikapanda kukuuza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Pamenepo anamangirira bulu mbereko, nati kwa mnyamata wake, Kusa, tiye; usandilezetsa kuyendaku, ndikapanda kukuuza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Pompo maiyo adaika chishalo nakwera bulu, ndipo adauza wantchitoyo kuti, “Thamangitsa buluyo. Usaleze mpaka ntakuuza.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Mayiyo anamangirira chishalo pa bulu ndipo anawuza wantchito wake kuti, “Yendetsa bulu mofulumira. Usachepetse liwiro pokhapokha nditakuwuza.”

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 4:24
7 Mawu Ofanana  

Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa namanga bulu wake, natengako anyamata ake awiri pamodzi naye, ndi Isaki mwana wake, nawaza nkhuni za nsembe yopsereza, nauka, nanka kumalo komwe Mulungu anamuuza iye.


Nanena ndi ana ake, Ndimangireni mbereko pabulu. Namangira iwo mbereko pabulu, naberekekapo iye.


Ndipo kunachitika, atadya iye mkate, ndi kumwa madzi, anammangira mbereko pabulu mneneri amene anambwezayo.


Ndipo anati, Ulikumuka kwa iye lero chifukwa ninji? Ngati mwezi wakhala, kapena mpa Sabata? Koma anati, Kuli bwino.


Potero anamuka, nafika kwa munthu wa Mulungu kuphiri la Karimele. Ndipo kunali, pakumuona munthu wa Mulungu alinkudza kutali, anati kwa Gehazi mnyamata wake, Tapenya, suyo Msunamu uja;


Pamenepo Mose anatenga mkazi wake ndi ana ake aamuna, nawakweza pabulu, nabwerera kunka ku dziko la Ejipito; ndipo Mose anagwira ndodo ya Mulungu m'dzanja lake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa