Mibadwo ya ana a Nowa, Semu, Hamu ndi Yafeti, ndi iyi; kwa iwo ndipo kunabadwa ana aamuna, chitapita chigumula chija.
Genesis 9:18 - Buku Lopatulika Ndi ana aamuna a Nowa amene anatuluka m'chingalawa ndiwo Semu, ndi Hamu, ndi Yafeti. Hamu ndiye atate wake wa Kanani. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndi ana amuna a Nowa amene anatuluka m'chingalawa ndiwo Semu, ndi Hamu, ndi Yafeti: Hamu ndiye atate wake wa Kanani. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ana a Nowa omwe adatuluka m'chombo muja anali Semu, Hamu ndi Yafeti. Hamu ndiye anali bambo wa Kanani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ana aamuna a Nowa amene anatuluka mʼchombo muja anali Semu, Hamu ndi Yafeti. Hamu anali abambo ake a Kanaani. |
Mibadwo ya ana a Nowa, Semu, Hamu ndi Yafeti, ndi iyi; kwa iwo ndipo kunabadwa ana aamuna, chitapita chigumula chija.
Ndipo Mulungu anati kwa Nowa, Ichi ndi chizindikiro cha pangano ndalikhazikitsa popangana ndi Ine ndi zamoyo zonse za padziko lapansi.
Semu ndi Yafeti ndipo anatenga chofunda, nachiika pa mapewa ao a onse awiri, nayenda chambuyo, nafunditsa umaliseche wa atate wao: nkhope zao zinali chambuyo, osaona umaliseche wa atate ao.