Genesis 8:4 - Buku Lopatulika Ndipo chingalawa chinaima pamapiri a Ararati, mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku lakhumi ndi asanu ndi awiri la mwezi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo chingalawa chinaima pa mapiri a Ararati, mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku lakhumi ndi asanu ndi awiri la mwezi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa ndipo pa tsiku la 17, mwezi wachisanu ndi chiŵiri, chombocho chidakaima pamwamba pa phiri la Ararati. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndipo pa tsiku la 17 la mwezi wachisanu ndi chiwiri, chombo chija chinakakhazikika pa mapiri a Ararati. |
Ndipo madzi analinkuchepa kufikira mwezi wakhumi; mwezi wakhumi tsiku loyamba mwezi ndipo padaoneka mitu ya mapiri.
Ndipo kunali popembedza iye m'nyumba ya Nisiroki mulungu wake, Adrameleki ndi Sarezere anamkantha ndi lupanga; napulumukira ku dziko la Ararati. Ndipo Esarahadoni mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.
Ndipo panali, pamene iye analikupembedzera m'nyumba ya Nisiroki, mulungu wake, Adrameleki ndi Sarezere, ana ake anamupha iye ndi lupanga; ndipo iwo anapulumuka, nathawira ku dziko la ku Ararati. Ndipo Esarahadoni, mwana wake, analamulira m'malo mwake.
Kwezani mbendera m'dziko, ombani lipenga mwa amitundu, konzerani amitundu amenyane naye, mummemezere maufumu a Ararati, Mini, ndi Asikenazi; muike nduna; amenyane naye; mukweretse akavalo ngati dzombe.