Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 8:4 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 ndipo pa tsiku la 17 la mwezi wachisanu ndi chiwiri, chombo chija chinakakhazikika pa mapiri a Ararati.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

4 Ndipo chingalawa chinaima pamapiri a Ararati, mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku lakhumi ndi asanu ndi awiri la mwezi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo chingalawa chinaima pa mapiri a Ararati, mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku lakhumi ndi asanu ndi awiri la mwezi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 ndipo pa tsiku la 17, mwezi wachisanu ndi chiŵiri, chombocho chidakaima pamwamba pa phiri la Ararati.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 8:4
6 Mawu Ofanana  

Madzi anakwera namiza mapiri kwa mamita pafupifupi asanu ndi awiri.


Madzi anapitirira kuphwa mpaka mwezi wa khumi, ndipo pa tsiku loyamba la mwezi wa khumiwo msonga za mapiri zinayamba kuonekera.


Tsiku lina, pamene Senakeribu ankapembedza mʼnyumba ya Nisiroki mulungu wake, ana ake Adirameleki ndi Sarezeri anamupha ndi lupanga ndipo anathawira ku dziko la Ararati. Tsono Esrahadoni, mwana wake, analowa ufumu mʼmalo mwake.


Tsiku lina, pamene ankapembedza mʼnyumba ya mulungu wake, Nisiroki, ana ake awiri, Adirameleki ndi Sarezeri anamupha ndi lupanga, ndipo anathawira mʼdziko la Ararati. Ndipo mwana wake Esrahadoni analowa ufumu mʼmalo mwake.


“Kwezani mbendera ya nkhondo mʼdziko! Lizani lipenga pakati pa mitundu ya anthu! Konzekeretsani mitundu ya anthu kuti ikamuthire nkhondo; itanani maufumu awa: Ararati, Mini ndi Asikenazi kuti adzamuthire nkhondo. Ikani mtsogoleri wankhondo kuti amenyane naye; tumizani akavalo ochuluka ngati magulu a dzombe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa