Ndipo panali pamene anapita masiku asanu ndi awiri, madzi a chigumula anali padziko lapansi.
Genesis 8:10 - Buku Lopatulika Ndipo analinda masiku ena asanu ndi awiri; natulutsanso njiwayo m'chingalawamo; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo analinda masiku ena asanu ndi awiri; natulutsanso njiwayo m'chingalawamo; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Atadikira masiku asanu ndi aŵiri ena, adaitulutsanso nkhunda ija m'chombo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho anadikirabe masiku ena asanu ndi awiri ndipo anatulutsanso nkhundayo mʼchombo muja. |
Ndipo panali pamene anapita masiku asanu ndi awiri, madzi a chigumula anali padziko lapansi.
Pakuti akapita masiku asanu ndi awiri Ine ndidzavumbitsa mvula padziko lapansi masiku makumi anai usana ndi usiku; ndi zinthu zamoyo zonse zomwe ndazipanga ndidzaziononga padziko lapansi.
ndipo njiwa inadza kwa iye madzulo; ndipo, taonani, m'kamwa mwake munali tsamba la azitona lothyoledwa: ndipo anadziwa Nowa kuti madzi analimkuphwa padziko lapansi.
Ndipo analindanso masiku ena asanu ndi awiri; natulutsa njiwayo: ndipo siinabwerenso konse kwa iye.
koma njiwayo siinapeze popondapo phazi lake, nibwera kwa iye kuchingalawako, pakuti madzi analipo padziko lonse lapansi; ndipo anatulutsa dzanja lake, naitenga, nailowetsa kwa iye m'chingalawamo.
Inde m'njira ya maweruziro anu, Yehova, ife talindira Inu; moyo wathu ukhumba dzina lanu, ndi chikumbukiro chanu.
Ndipo ndidzalindira Yehova, amene wabisira a nyumba ya Yakobo nkhope yake, ndipo ndidzamyembekeza Iye.