Genesis 8:11 - Buku Lopatulika11 ndipo njiwa inadza kwa iye madzulo; ndipo, taonani, m'kamwa mwake munali tsamba la azitona lothyoledwa: ndipo anadziwa Nowa kuti madzi analimkuphwa padziko lapansi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201411 ndipo njiwa inadza kwa iye madzulo; ndipo, taonani, m'kamwa mwake munali tsamba la azitona lothyoledwa: ndipo anadziwa Nowa kuti madzi analimkuphwa pa dziko lapansi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa11 Madzulo idabwerako, ndipo Nowa adaona kuti kukamwa kwake kuli tsamba laliŵisi la mtengo wa olivi. Apo Nowa adadziŵa kuti madzi ayamba kuphwa. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero11 Pamene nkhunda inabwerera madzulo ake, inali itanyamula tsamba laliwisi la mtengo wa olivi. Motero Nowa anadziwa kuti madzi aphwadi pa dziko lapansi. Onani mutuwo |
ndi kuti azilalikira ndi kumveketsa m'midzi mwao monse ndi mu Yerusalemu, ndi kuti, Muzitulukira kuphiri, ndi kutengako nthambi za azitona, ndi nthambi za mitengo yamafuta, ndi nthambi za mitengo yamchisu, ndi zinkhwamba za migwalangwa, ndi nthambi za mitengo zothonana, kumanga nazo misasa monga munalembedwa.