Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 7:7 - Buku Lopatulika

Ndipo analowa Nowa ndi ana ake ndi mkazi wake ndi akazi a ana ake m'chingalawamo, chifukwa cha madzi a chigumula.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo analowa Nowa ndi ana ake ndi mkazi wake ndi akazi a ana ake m'chingalawamo, chifukwa cha madzi a chigumula.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Iyeyo ndi mkazi wake ndi ana ake aamuna ndi akazi ao adaloŵa m'chombo, kuthaŵa chigumulacho.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ndipo Nowa, ana ake aamuna, mkazi wake, pamodzi ndi ana ake aakazi analowa mu chombo chija kuthawa madzi a chigumula.

Onani mutuwo



Genesis 7:7
10 Mawu Ofanana  

Koma ndidzakhazikitsa ndi iwe pangano langa; ndipo udzalowa m'chingalawamo iwe ndi ana ako ndi mkazi wako, ndi akazi a ana ako pamodzi ndi iwe.


Ndipo anati Yehova kwa Nowa, Talowani, iwe ndi akunyumba ako onse m'chingalawamo; chifukwa ndakuona iwe kuti uli wolungama pamaso panga m'mbadwo uno.


Wochenjera aona zoipa, nabisala; koma achibwana angopitirira, nalipitsidwa.


Pakuti monga m'masiku aja, chisanafike chigumula, anthu analinkudya ndi kumwa, analikukwatira ndi kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analowa m'chingalawa,


Anadya, anamwa, anakwatira, anakwatiwa, kufikira tsiku lija Nowa analowa m'chingalawa, ndipo chinadza chigumula, nkuwaononga onsewo.


Ndi chikhulupiriro Nowa, pochenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zisanapenyeke, ndi pochita mantha, anamanga chingalawa cha kupulumutsiramo iwo a m'nyumba yake; kumene anatsutsa nako dziko lapansi, nakhala wolowa nyumba wa chilungamo chili monga mwa chikhulupiriro.


kuti mwa zinthu ziwiri zosasinthika, m'mene Mulungu sangathe kunama, tikakhale nacho chotichenjeza cholimba, ife amene tidathawira kuchigwira chiyembekezo choikika pamaso pathu;


imene inakhala yosamvera kale, pamene kuleza mtima kwa Mulungu kunalindira, m'masiku a Nowa, pokhala m'kukonzeka chingalawa, m'menemo owerengeka, ndiwo amoyo asanu ndi atatu, anapulumutsidwa mwa madzi;


ndipo sanalekerere dziko lapansi lakale, koma anasunga Nowa mlaliki wa chilungamo, ndi anzake asanu ndi awiri, pakulitengera dziko la osapembedza chigumula;