Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 7:7 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Ndipo Nowa, ana ake aamuna, mkazi wake, pamodzi ndi ana ake aakazi analowa mu chombo chija kuthawa madzi a chigumula.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

7 Ndipo analowa Nowa ndi ana ake ndi mkazi wake ndi akazi a ana ake m'chingalawamo, chifukwa cha madzi a chigumula.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo analowa Nowa ndi ana ake ndi mkazi wake ndi akazi a ana ake m'chingalawamo, chifukwa cha madzi a chigumula.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Iyeyo ndi mkazi wake ndi ana ake aamuna ndi akazi ao adaloŵa m'chombo, kuthaŵa chigumulacho.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 7:7
10 Mawu Ofanana  

Koma ndidzachita pangano langa ndi iwe. Iwe, ana ako aamuna, mkazi wako ndi akazi a ana ako nonse mudzalowa mʼchombocho.


Ndipo Yehova anati kwa Nowa, “Lowa mu chombo iwe ndi banja lako lonse, chifukwa ndaona kuti ndiwe wolungama mu mʼbado uwu.


Munthu wochenjera akaona choopsa amabisala, koma munthu wopusa amangopitirira ndipo amadzanongʼoneza bondo.


Pakuti masiku amenewo chisanafike chigumula, anthu amadya ndi kumwa, kukwatira ndi kukwatiwa, mpaka tsiku limene Nowa analowa mʼchombo;


Anthu ankadya, kumwa, kukwatira ndi kukwatiwa mpaka tsiku limene Nowa analowa mʼchombo. Pomwepo chigumula chinafika ndi kuwawononga onsewo.


Ndi chikhulupiriro, Nowa atachenjezedwa za zinthu zimene zinali zisanaoneke, anachita mantha napanga chombo kuti apulumutsire banja lake. Ndi chikhulupiriro chake anatsutsa dziko lapansi ndipo analandira chilungamo chimene chimabwera ndi chikhulupiriro.


Mulungu anachita zinthu ziwiri, lonjezo ndi lumbiro, zimene sizingathe kusintha ndipo Mulungu sangathe kunama. Choncho Mulungu akutilimbikitsa mtima ife amene tinathawira kwa Iye kuti tichigwiritsitse chiyembekezo chimene tinalandira.


ya anthu amene sanamvere Mulungu atadikira moleza mtima pa nthawi imene Nowa ankapanga chombo. Mʼchombo chija anthu owerengeka okha, asanu ndi atatu, ndiwo anapulumutsidwa ku madzi.


Iye sanalekerere dziko lapansi kalelo, koma anapulumutsa Nowa, mlaliki wa chilungamo, ndi anthu ena asanu ndi awiri atadzetsa chigumula pa dziko lapansi kwa anthu akhalidwe losapembedza Mulunguyo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa