Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 17:27 - Buku Lopatulika

27 Anadya, anamwa, anakwatira, anakwatiwa, kufikira tsiku lija Nowa analowa m'chingalawa, ndipo chinadza chigumula, nkuwaononga onsewo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Anadya, anamwa, anakwatira, anakwatiwa, kufikira tsiku lija Nowa analowa m'chingalawa, ndipo chinadza chigumula, nichiwaononga onsewo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Masiku amenewo anthu ankangodya ndi kumwa, ankakwatira ndi kumakwatiwa, mpaka tsiku limene Nowa adaloŵa m'chombo. Pamenepo chigumula chidafika nkuŵaononga onse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Anthu ankadya, kumwa, kukwatira ndi kukwatiwa mpaka tsiku limene Nowa analowa mʼchombo. Pomwepo chigumula chinafika ndi kuwawononga onsewo.

Onani mutuwo Koperani




Luka 17:27
16 Mawu Ofanana  

Ndipo zinaonongedwa zamoyo zonse zimene zinali padziko lapansi, anthu, ndi nyama, ndi zokwawa, ndi mbalame za m'mlengalenga; ndipo zinaonongedwa padziko lapansi: anatsala Nowa yekha ndi amene anali pamodzi naye m'chingalawa.


Ndipo analowa Nowa ndi ana ake ndi mkazi wake ndi akazi a ana ake m'chingalawamo, chifukwa cha madzi a chigumula.


Mtima wanga uguguda, mantha andiopsetsa ine; chizirezire chimene ndinachikhumba chandisandukira kunthunthumira.


Chifukwa chake choipa chidzafika pa iwe; sudzadziwa kucha kwake, ndipo chionongeko chidzakugwera; sudzatha kuchikankhira kumbali; ndipo chipasuko chosachidziwa iwe chidzakugwera mwadzidzidzi.


Pakuti m'kuuka kwa akufa sakwatira, kapena kukwatiwa, koma akhala ngati angelo a Kumwamba.


Ndipo monga kunakhala masiku a Nowa, momwemo kudzakhalanso masiku a Mwana wa Munthu.


Monga momwenso kunakhala masiku a Loti; anadya, anamwa, anagula, anagulitsa, anabzala, anamanga nyumba;


Ndipo pamene anatsika naye, onani, iwo anabalalika apo ponse, analinkudya, ndi kumwa, ndi kudyerera, chifukwa cha chofunkha zambiri anazitenga ku dziko la Afilisti, ndi ku dziko la Yuda.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa