Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 50:9 - Buku Lopatulika

Ndipo anakwera pamodzi ndi iye magaleta ndi apakavalo; ndipo panali khamu lalikulu.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo anakwera pamodzi ndi iye magaleta ndi apakavalo; ndipo panali khamu lalikulu.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Asilikali okwera pa magaleta ndi akavalo, nawonso adamperekeza. Motero chinali chinamtindi cha anthu.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Asilikali okwera pa magaleta ndi asilikali a pa akavalo anapita nayenso pamodzi. Linali gulu lalikulu.

Onani mutuwo



Genesis 50:9
10 Mawu Ofanana  

ndipo anamkweza iye m'galeta wake wachiwiri amene anali naye: ndipo anafuula patsogolo pa iye, Gwadani; ndipo anamkhazika iye wolamulira dziko lonse la Ejipito.


Ndipo Yosefe anamanga galeta lake nakwera kunka kukakomana naye Israele atate wake, ku Goseni, ndipo anadzionetsera yekha kwa iye, nagwera pakhosi pake nakhala m'kulira pakhosi pake.


Ndipo anafika pa dwale la Atadi, lili tsidya lija la Yordani, pamenepo anamlira maliro a atate wake masiku asanu ndi limodzi.


ndi mbumba yonse ya Yosefe ndi abale ake, ndi mbumba ya atate wake: ang'ono ao okha, ndi nkhosa zao, ndi ng'ombe zao, anazisiya m'dziko la Goseni.


Posakhoza kutero, mudzabweza bwanji nkhope ya nduna imodzi ya anyamata aang'ono a mbuye wanga, ndi kukhulupirira Ejipito akupatse magaleta ndi apakavalo?


Ndipo Ine, taonani, ndidzalimbitsa mitima ya Aejipito, kuti alowemo powatsata; ndipo ndidzalemekezedwa pa Farao, ndi pa nkhondo yake yonse, pa magaleta ake, ndi pa okwera pa akavalo ake.


Popeza madziwo anabwerera, namiza magaleta ndi apakavalo, ndiwo nkhondo yonse ya Farao imene idalowa pambuyo pao m'nyanja; sanatsale wa iwowa ndi mmodzi yense.


napita nao magaleta osankhika mazana asanu ndi limodzi, ndi magaleta onse a mu Ejipito, ndi akapitao ao onse.


Ndakulinganiza, wokondedwa wanga mnyamatawe, ngati akavalo a magaleta a Farao.


Ndipo anamuika Stefano anthu opembedza, namlira maliro aakulu.