Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 49:2 - Buku Lopatulika

Sonkhanani, tamvani, ana aamuna a Yakobo; tamverani Israele atate wanu.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Sonkhanani, tamvani, ana amuna a Yakobo; tamverani Israele atate wanu.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

“Bwerani kuno, ndipo mumve, inu ana a Yakobe, mverani bambo wanu Israele.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

“Bwerani ndipo imvani mawu anga, inu ana a Yakobo; mverani abambo anu Israeli.

Onani mutuwo



Genesis 49:2
13 Mawu Ofanana  

Rubeni, ndiwe woyamba wanga, mphamvu yanga ndi chiyambi cha mphamvu yanga; ulemu wopambana, ndi mphamvu yopambana.


Idzani ananu ndimvereni ine, ndidzakulangizani zakumuopa Yehova.


Munthu wokhumba moyo ndani, wokonda masiku, kuti aone zabwino?


Tamvera atate wako anakubala, usapeputse amai ako atakalamba.


Mwananga, undipatse mtima wako, maso ako akondwere ndi njira zanga.


Mwananga, mvera nzeru yanga; tcherera makutu ku luntha langa;


Mwananga, sunga malangizo a atate wako, usasiye malamulo a mai ako;


Mwananga, sunga mau anga, ukundike malangizo anga,


Ndipo tsopano, ananga, mundimvere ine, labadirani mau a m'kamwa mwanga.


Ndipo tsopano, ananga, mundimvere ine, ngodala akusunga njira zanga.


Sonkhanani inu nonse ndi kumva, ndani mwa iwo aonetsa zinthu izi? Iye amene Yehova anamkonda, iye adzachita kufuna kwake pa Babiloni, ndi mkono wake udzakhala pa Ababiloni.