Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 34:12 - Buku Lopatulika

12 Munthu wokhumba moyo ndani, wokonda masiku, kuti aone zabwino?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Munthu wokhumba moyo ndani, wokonda masiku, kuti aone zabwino?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Ndani mwa inu amakhumba moyo ndi kulakalaka kuti akhale masiku ambiri, kuti asangalale ndi zinthu zabwino?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Aliyense wa inu amene amakonda moyo wake ndi kukhumba kuti aone masiku abwino ambiri,

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 34:12
16 Mawu Ofanana  

Sonkhanani, tamvani, ana aamuna a Yakobo; tamverani Israele atate wanu.


Ngati mulibe mau, tamverani ine; mukhale chete, ndipo ndidzakuphunzitsani nzeru.


Kumbukira kuti moyo wanga ndiwo mphepo, diso langa silidzaonanso chokoma.


Anakupemphani moyo, mwampatsa iye; mwamtalikitsira masiku kunthawi za nthawi.


Ambiri amati, Adzationetsa chabwino ndani? Weramutsirani ife kuunika kwa nkhope yanu, Yehova.


Ndidzamkhutitsa ndi masiku ambiri, ndi kumuonetsera chipulumutso changa.


Mwananga, tamvera mau anga; tcherera makutu ku zonena zanga.


Ndipo tsopano, ananga, mundimvere ine, labadirani mau a m'kamwa mwanga.


Chiyambi cha nzeru ndicho kuopa Yehova; kudziwa Woyerayo ndiko luntha.


Mau atha; zonse zamveka zatha; opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.


Ndinafuna mumtima mwanga kusangalatsa thupi langa ndi vinyo, mtima wanga ulikunditsogolera mwanzeru, ndi kugwira utsiru, kuti ndizindikire chabwinocho cha ana a anthu nchiyani chimene azichichita pansi pa thambo masiku onse a moyo wao.


Ndiponso kuti munthu yense adye namwe naone zabwino m'ntchito zake zonse; ndiwo mtulo wa Mulungu.


kukonda Yehova Mulungu wanu, kumvera mau ake, ndi kummamatira Iye, pakuti Iye ndiye moyo wanu, ndi masiku anu ochuluka; kuti mukhale m'dziko limene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo, kuwapatsa ili.


kuti muope Yehova Mulungu wanu, kusunga malemba ake onse ndi malamulo ake, amene ndikuuzani inu ndi ana anu, ndi zidzukulu zanu, masiku onse a moyo wanu, ndi kuti masiku anu achuluke.


Ndipo inenso, kukhale kutali ndi ine, kuchimwira Yehova ndi kuleka kukupemphererani; koma ndidzakulangizani njira yabwino ndi yolungama.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa