Ndipo anabalanso mphwake Abele. Abele anakhala mbusa wa nkhosa, koma Kaini anali wakulima nthaka.
Genesis 47:3 - Buku Lopatulika Ndipo Farao anati kwa abale ake, Ntchito yanu njotani? Ndipo iwo anati kwa Farao, Akapolo anu ndi abusa, ife ndi atate athu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Farao anati kwa abale ake, Ntchito yanu njotani? Ndipo iwo anati kwa Farao, Akapolo anu ndi abusa, ife ndi atate athu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Farao adaŵafunsa kuti, “Kodi mumagwira ntchito yanji?” Iwo adayankha kuti, “Ndife abusa bwana, monga momwe ankachitira makolo athu.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Farao anafunsa abale akewo kuti, “Mumagwira ntchito yanji?” Iwo anamuyankha kuti, “Ife, bwana ndife oweta ziweto, monga ankachitira makolo athu. |
Ndipo anabalanso mphwake Abele. Abele anakhala mbusa wa nkhosa, koma Kaini anali wakulima nthaka.
Pamenepo anati kwa iye, Utiuzetu choipa ichi chatigwera chifukwa cha yani? Ntchito yako njotani? Ufuma kuti? Dziko lako nliti? Nanga mtundu wako?
Pakutinso pamene tinali nanu tidakulamulirani ichi, Ngati munthu safuna kugwira ntchito, asadyenso.